KUIZUKUTA MANePS
November 06, 2026

ZOKAMBIRANA

Pamene Ntchito yolimbikitsa  ochita malonda komanso nthambi zaboma m’dziko muno kuti zizigwiritsa ntchito ndondomeko yatsopano ya makina a intaneti  yogulira komanso kugulitsira katundu waboma ya Malawi National Electronic Procurement System (MANePS) ikupitilira, ofesi ya PPDA sabata yangothayi inali muchigawo chakumpoto kumene inabweretsa pamodzi nthambi  zaboma komanso ochita malonda mumzinda wa Mzuzu ndi madera ozungulira, pofuna kumva maganizo awo, zammene akuyionera MANePS.


Chosangalatsa ndichakuti ambiri mwaiwo akukondwera nayo  MANePS, ponena kuti mwazina yachepetsa nthawi yomwe amatenga pofuna kugula katundu, komanso kuti chinyengo chichepa.


Mkulu wa ofesi ya PPDA a George Mankhwala analimbikitsa  anthu omwe anbwera ku zokambiranazi kuti akhale akazembe a MANePS, potsindika kuti MANePS yabwera kuzathandiza kuteteza chuma chaboma. 


Ena mwamaofesi aboma omwe anali pamkumanowo ndi Mzuzu Central Hospital, Mzuzu Technical College. Mzuzu University, Northen region water Board, Mzuzu City Council, Northern Education Division komanso Mzuzu ADD.